Proverbs 11:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kulungama kwa munthu woyera mtima kumampulumutsa, koma zilakolako zoipa zimaŵaika mu ukapolo anthu onyenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa, koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cilungamo ca oongoka mtima cidzawapulumutsa; Koma aciwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.