Proverbs 12:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu woyankhula mosasamala mawu ake amalasa ngati lupanga, koma mawu a munthu wanzeru amachiritsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; Koma lilime la anzeru lilamitsa.