Proverbs 12:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wake; koma wochititsa manyazi akunga chovunditsa mafupa a mwamunayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi wakhalidwe labwino ali ngati chipewa chaufumu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda cha mafinya kwa mwamuna wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi wodekha ndiye korona wa mwamuna wace; Koma wocititsa manyazi akunga cobvunditsa mafupa a mwamunayo.