Proverbs 13:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; koma wonyoza samvera chidzudzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wanzeru amamvera malangizo a abambo ake, koma mwana wonyoza samamvetsera chidzudzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwana wanzeru amamvera mwambo wa atate; Koma wonyoza samvera cidzudzulo.