Proverbs 14:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima umadziŵa wokha zoŵaŵa zake, ndipo palibe wina angadziŵe kukondwa kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima udziwa kuwawa kwakekwake; mlendo sadudukira ndi chimwemwe chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake, ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima udziwa kuwawa kwace kwace; Mlendo sadudukira ndi cimwemwe cace.