Proverbs 18:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu. Koma chimangolankhula za maganizo ake okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wopusa sakondwera ndi kuzindikira; koma kungovumbulutsa za m'mtima mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chitsiru chilibe chidwi chomvetsa zinthu, koma chimakondwera ndi kuyankhula maganizo ake okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wopusa sakondwera ndi kuzindikira; Koma kungobvumbulutsa za m'mtima mwace.