Proverbs 19:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nzeru zimapangitsa munthu kukhala wosakwiya msanga; ulemerero wake uli posalabadira kuchitiridwa zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kulingalira kwa munthu kucedwetsa mkwiyo; Ulemerero wace uli wakuti akhululukire colakwa.