Proverbs 21:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wonyoza akalangidwa, wopusapusa amaphunzirapo nzeru. Munthu wanzeru akamlangiza, amamvetsa zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru, naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wonyoza akalangidwa, anthu opusa amapeza nzeru; koma munthu wanzeru akalangizidwa, amapeza chidziwitso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru, Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.