Proverbs 21:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake; koma Yehova ayesa mitima.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Makhalidwe a munthu amaoneka olungama kwa mwini wakeyo, koma Yehova ndiye amayesa mtima wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace; Koma Yehova ayesa mitima.