Proverbs 22:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'njira ya munthu wosalungama muli minga ndi misampha, koma wodzisamala bwino adzazilewa zonsezo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Minga ndi misampha ili m'njira ya wokhota; koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼnjira za anthu oyipa muli minga ndi misampha, koma amene amasala moyo wake adzazipewa zonsezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Minga ndi misampha iri m'njira ya wokhota; Koma wosunga moyo wace adzatarikira imeneyo.