Proverbs 23:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe udzati, “Adanditchaya, koma sadandipweteke. Adandimenya, koma ine osamvako. Kodi ine ndidzatsitsimuka liti? Ndiye ndithamangira chakumwa china.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; anandikwapula, osamva ine; ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafunafunanso vinyoyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe udzanena kuti, “Anandimenya, koma sindinapwetekedwe! Andimenya koma sindinamve kanthu! Kodi ndidzuka nthawi yanji? Ndiye ndifunefunenso vinyo wina.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine; Anandikwapula, osamva ine; Ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafuna-funanso vinyoyo.