Proverbs 23:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja iye amangokhalira kuganiza za mtengo wa zinthu. Amakuuza kuti, “Kazidya, kazimwa!” Koma mumtima mwake zimenezo sakuzifuna.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
paja iye ndi munthu amene nthawi zonse amaganizira za mtengo wake ngakhale amati kwa iwe, “Idya ndi kumwa,” koma sakondweretsedwa nawe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti monga asinkha m'kati mwace, ali wotere; Ati kwa iwe, Idya numwe; Koma mtima wace suli pa iwe.