Proverbs 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udziwe kuti nzeru ndi yoteronso pa moyo wako; ngati uyipeza nzeruyo, zinthu zidzakuyendera bwino mʼtsogolo, ndipo chiyembekezo chako sichidzapita pachabe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero udzadziwa kuti nzeru iri yotero m'moyo wako; Ngati waipeza padzakhala mphotho, Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.