Proverbs 25:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa munthu womvetsa bwino, kudzudzula kwa munthu wanzeru kuli ngati ndolo zagolide kapena chodzikongoletsera china cha golide wabwino kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga phelele lagolidi ndi cipini cagolidi woyengeka, Momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.