Proverbs 25:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukhulupirira munthu wosakhulupirika pa nthaŵi yamavuto kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa, kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kukhulupirira munthu wa chiwembu tsiku latsoka kunga dzino lothyoka ndi phazi loguluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kudalira munthu wosankhulupirika pa nthawi ya mavuto, kuli ngati dzino lobowoka kapena phazi lolumala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kukhulupirira munthu wa ciwembu tsiku latsoka Kunga dzino lotyoka ndi phazi loguluka.