Proverbs 25:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kumvula zovala pa nyengo yachisanu, ndiponso ngati kumthira vinyo wosasa pa chilonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga wovula malaya tsiku lamphepo, ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, momwemo woimbira nyimbo munthu wachisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyimbira nyimbo munthu wachisoni kuli ngati kuvula zovala pa nyengo yozizira kapena kuthira mchere pa chilonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga wobvula maraya tsiku lamphepo, Ngakhale kuthira vinyo wosasa m'soda, Momwemo woyimbira nyimbo munthu wacisoni.