Proverbs 26:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga miyendo ya munthu wopunduka imakhala yopanda ntchito, ndimonso umakhalira mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Miyendo ya wopunduka ili yolobodoka, momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvu ndi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Miyendo ya wopunduka iri yolobodoka, Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.