Proverbs 27:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la atate ako. Usachite kupita ku nyumba ya mbale wake, ukakhala pa mavuto. Mnzako wokhala naye pafupi amaposa mbale wako wokhala kutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mnzako, ndi mnzake wa atate wako, usawasiye; usanke kunyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; mnansi wapafupi aposa mbale wakutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako, ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto; mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mnzako, ndi mnzace wa atate wako, usawasiye; Usanke ku nyumba ya mbale wako tsiku la tsoka lako; Mnansi wapafupi aposa mbale wakutari.