Proverbs 28:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene amasokeza anthu olungama kuti azitsata njira yoipa, adzagwa m'dzenje lake lomwe. Koma anthu amene alibe cholakwa adzalandira choloŵa chabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amene amatsogolera anthu olungama kuti ayende mʼnjira yoyipa adzagwera mu msampha wake womwe, koma anthu opanda cholakwa adzalandira cholowa chabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wosoceretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, Adzagwa mwini m'dzenje lace; Koma angwiro adzalandira colowa cabwino.