Proverbs 28:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wolemera amadziyesa wanzeru, koma munthu wosauka amene ali womvetsa zinthu, amamtulukira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolemera adziyesa wanzeru; koma wosauka wozindikira aululitsa zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wolemera amadziyesa kuti ndi wanzeru, koma munthu wosauka amene ali ndi nzeru zodziwa zinthu amamutulukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolemera adziyesa wanzeru; Koma wosauka wozindikira aululitsa zace.