Proverbs 28:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Eni dziko akachita zaupandu, oŵalamulira amachuluka. Koma anthu akakhala omvetsa ndi odziŵa zinthu, dzikolo limakhazikika nthaŵi yaitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mʼdziko muli kuwukirana, dzikolo limakhala ndi olamulira ambiri, koma anthu omvetsa ndi odziwa zinthu bwino ndiwo angakhazikitse bata mʼdzikolo nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pocimwa dziko akalonga ace acuruka; Koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikuru.