Proverbs 29:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira aŵakomere mtima, koma munthu amamuweruza molungama ndi Chauta yekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambiri afunafuna chiyanjano cha mkulu; koma chiweruzo cha munthu chichokera kwa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ambiri amafunitsitsa kuti wolamulira awakomere mtima, koma munthu amaweruzidwa mwachilungamo ndi thandizo la Yehova basi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambiri afunafuna ciyanjano ca mkuru; Koma ciweruzo ca munthu cicokera kwa Yehova.