Proverbs 30:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pali ena amene amasongola mano ao ngati malupanga, amaŵanola ngati mipeni, kuti adye amphaŵi ndi kuŵachotsa pa dziko lapansi, kutinso achotse anthu osauka pakati pa anzao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; kuti adye osauka kuwachotsa kudziko, ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga ndipo zibwano zawo zili ngati mipeni moti amadya amphawi ndi kuwachotsa pa dziko lapansi. Amachotsanso anthu osauka pakati pa anzawo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni; Kuti adye osauka kuwacotsa kudziko, ndi aumphawi kuwacotsa mwa anthu.