Proverbs 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtsundu uli ndi ana aakazi aŵiri. Anawo amangokhalira kulira kuti, “Tipatseni chakuti, tipatseni chakuti.” Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta. Pali zinthu zinai zimene siziti, “Takwana.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa. Pali zinthu zitatu sizikhuta konse, ngakhale zinai sizinena, Kwatha:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Msundu uli ndi ana aakazi awiri iwo amalira kuti, ‘Tipatseni! Tipatseni!’ ” “Pali zinthu zitatu zimene sizikhuta, zinthu zinayi zimene sizinena kuti, ‘Takhuta!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa, Pali zinthu zitatu sizikhuta konse, Ngakhale zinai sizinena, Kwatha: