Proverbs 30:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense amene amaseka bambo ndi kumanyozera kumvera mai, makwangwala akuchigwa adzamkoloola maso, ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense amene amanyoza abambo ake, ndi kunyozera kumvera amayi ake, makwangwala a ku chigwa adzamukolowola maso ndipo mphungu zidzadya mnofu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Diso locitira atate wace ciphwete, ndi kunyoza kumvera amace, Makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya,