Proverbs 30:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja ukakuntha mkaka, mafuta amapangika. Ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo ukautsa mkwiyo, mikangano imaoneka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo; ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo, ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa, ndipo ukapsinya mphuno, magazi amatuluka, ndipo mikangano imakhalapo ukalimbikira kukwiya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo; Ndi popsinja mpfuno, mwazi uturukamo; Ndi potimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.