Proverbs 30:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani adaakwera kumwamba natsikako? Ndani adafumbatapo mphepo m'manja? Ndani adafukusapo madzi m'chovala? Ndani adakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani, ndipo mwana wake dzina lake ndani? Tanenatu ngati ukudziŵa!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'malaya ake? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako? Ndani anafumbatapo mphepo mʼmanja mwake? Ndani anamanga madzi mʼchovala chake? Ndani anakhazikitsa mathero onse a dziko lapansi? Dzina lake ndani? Ndiwuze ngati ukudziwa! Ndipo mwana wake dzina lake ndani?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndani anakwera kumwamba natsikanso? Ndani wakundika nafumbata mphepo? Ndani wamanga madzi m'maraya ace? Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko? Dzina lace ndani? dzina la mwanace ndani? kapena udziwa.