Proverbs 31:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu amene ali pafupi kufa, uzimpatsa chakumwa chaukali, ndipo munthu amene ali pa mavuto oopsa, uzimpatsa vinyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wofuna kufa umpatse chakumwa chaukali, ndi vinyo kwa owawa mtima;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Perekani chakumwa choledzeretsa kwa amene ali pafupi kufa, vinyo kwa amene ali pa mavuto woopsa;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wofuna kufa umpatse cakumwa caukali, Ndi vinyo kwa owawa mtima;