Proverbs 4:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka dzuwa litafika pa mutu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca, Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.