Proverbs 6:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi ndipo mkazi wa mwini wake amasokonezeratu moyo wako wonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamariza ndi nyenyeswa; Ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatari.