Proverbs 6:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe ikangogwidwa, imalipira kasanunkaŵiri, mpaka mwina kulandidwa katundu yense wa m'nyumba mwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri, ngakhale kulandidwa katundu wa mʼnyumba mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; Idzapereka cuma conse ca m'nyumba yace.