Psalms 10:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inutu mumaonadi, mumazindikira zovuta ndi zosautsa, kuti muchitepo kanthu. Wopanda mwai amadzipereka kwa Inu. Nayenso wamasiye mumamthandiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa, mumaganizira zochitapo kanthu. Wovutikayo amadzipereka yekha kwa Inu pakuti Inu ndi mthandizi wa ana amasiye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwapenya; pakuti mumayang'anira cibvutitso ndi cisoni kuti acipereke m'manja mwanu; Waumphawi adzipereka kwa Inu; Wamasiye mumakhala mthandizi wace.