Psalms 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakamwa pake pamangolankhula zotemberera, zonyenga ndi zoopseza. M'kamwa mwake mumatuluka zovutitsa ena ndiponso zoipa zokhazokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza; zovutitsa ndi zoyipa zili pansi pa lilime lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kamwa mwace mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kucenjerera; Pansi pa lilime lace pali cibvutitso copanda pace.