Psalms 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amabisalira osauka ngati mkango m'ngaka yake, amabisalira osauka kuti aŵagwire. Osaukawo amaŵagwiradi akaŵakokera mu ukonde wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alalira monga mkango m'ngaka mwake; alalira kugwira wozunzika, agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba. Amabisalira kuti agwire anthu opanda mphamvu; amagwira anthu opanda mphamvu ndi kuwakokera mu ukonde wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alalira monga mkango m'ngaka mwace; Alalira kugwira wozunzika: Agwira wozunzika, pakumkola m'ukonde mwace.