Psalms 101:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzatsata njira yopanda cholakwa. Nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzakhala ndi mtima wangwiro m'nyumba mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzachita mwanzeru m'njira yangwiro; mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzacita mwanzeru m'njira yangwiro; Mudzandidzera liti? Ndidzayenda m'nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.