Psalms 104:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu, mafuta amene amachititsa nkhope yake kuwala, ndi buledi amene amapereka mphamvu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, Ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yace, Ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.