Psalms 106:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tipulumutseni Inu Chauta, Mulungu wathu, mutisonkhanitse kuchokera pakati pa anthu akunja, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, kuti tizinyadira pokutamandani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, ndi kutisokolotsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tipulumutseni Inu Yehova Mulungu wathu, ndipo mutisonkhanitse kuchoka kwa anthu a mitundu ina kuti tithe kuyamika dzina lanu loyera ndi kunyadira mʼmatamando anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, Ndi kutisokolotsa kwa amitundu, Kuti tiyamike dzina lanu loyera, Ndi kudzitamandira naco cilemekezo canu.