Psalms 106:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene makolo athu anali ku Ejipito, sadasamale ntchito zanu zodabwitsa. Sadakumbukire kukula kwa chikondi chanu chosasinthika, koma adaukira Mulungu Wopambanazonse ku Nyanja Yofiira kuja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Makolo athu sanadziwitse zodabwitsa zanu m'Ejipito; sanakumbukire zachifundo zanu zaunyinji; koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene makolo athu anali mu Igupto, sanalingalire za zozizwitsa zanu; iwo sanakumbukire kukoma mtima kwanu kochuluka, ndipo anawukira Inu pa Nyanja Yofiira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Makolo athu sanadziwitsa zodabwiza zanu m'Aigupto; Sanakumbukila zacifundo zanu zaunyinji; Koma anapikisana ndi Inu kunyanja, ku Nyanja Yofiira.