Psalms 109:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti munthuyo sadakumbukire kuchita chifundo, koma adazunza osauka, osoŵa ndi ovutika mu mtima, mpaka kuŵapha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti iye sanaganizirepo zochita chifundo, koma anazunza mpaka kuwapha anthu osauka ndi osweka mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti sanakumbukila kucita cifundo, Koma analondola wozunzika ndi waumphawi, Ndi wosweka mtima, kuti awaphe.