Psalms 112:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; adzakukuta mano, nadzasungunuka; chokhumba oipa chidzatayika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu woyipa adzaona zimenezi ndipo adzapsa mtima; adzakukuta mano ake ndipo adzasungunuka. Zolakalaka za anthu oyipa sizidzachitika konse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Woipa adzaziona, nadzapsa mtima; Adzakukuta mano, nadzasungunuka; Cokhumba oipa cidzatayika.