Psalms 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thandizeni, Inu Chauta, palibenso munthu wosamala za Inu, okhulupirika sapezekanso pakati pa anthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Seminiti. Salimo la Davide. Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika; okhulupirika akusowa pakati pa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; Pakuti okhulupirika acepa mwa ana a anthu.