Psalms 12:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa choti osauka alandidwa zao ndipo osoŵa akudandaula, Chauta akunena kuti, “Ndichitapo kanthu tsopano, ndiŵapulumutsa monga momwe akufuniramo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvu ndi kubuwula kwa anthu osowa, Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova, “Ndidzawateteza kwa owazunza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca kupasuka kwa ozunzika, cifukwa ca kuusa moyo kwa aumphawi, Ndiuka tsopano, ati Yehova; Ndidzamlonga mosungika muja alaka-lakamo.