Psalms 123:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Monga momwe anyamata amayang'anira ku dzanja la bwana wao, monga momwe adzakazi amayang'anira ku dzanja la dona wao, ndi momwenso timayang'anira ife kwa Chauta Mulungu wathu, mpaka atatichitira chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la mbuye wao, monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, kufikira atichitira chifundo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, monga momwe maso a akapolo amayangʼana mʼdzanja la mbuye wawo, monga momwenso maso a mdzakazi amayangʼana mʼdzanja la dona wake, choncho maso athu ali kwa Yehova Mulungu wathu, mpaka atichitire chifundo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, monga maso a anyamata ayang'anira dzanja la ambuye ao, Monga maso a adzakazi ayang'anira dzanja la mbuye wao wamkazi: Momwemo maso athu ayang'anira Yehova Mulungu wathu, Kufikira aticitira cifundo.