Psalms 125:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu oipa sadzalamulira nthaŵi yonse dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake, kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndodo yacifumu ya coipa siidzapumula pa gawo la olungama; Kuti olungama asaturutse dzanja lao kucita cosalungama,