Psalms 126:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo tidasekera kwambiri, ndipo tidalulutira ndi chimwemwe. Tsono mitundu ina ya anthu inkanena kuti, “Chauta waŵachitira zazikulu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, ndi lilime lathu linafuula mokondwera; pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawachitira iwo zazikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka; malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe. Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti, “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo pakamwa pathu panadzala ndi kuseka, Ndi lilime lathu linapfuula mokondwera; Pamenepo anati mwa amitundu, Yehova anawacitira iwo zazikuru,