Psalms 127:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa ndi kukagona mochedwa, kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya. Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao iwowo ali m'tulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuli chabe kwa inu kulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, kudya mkate wosautsa kuupeza; kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ake ngati m'tulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumangodzivuta nʼkulawirira mmamawa ndi kusagona msanga madzulo, kuvutikira chakudya choti mudye, pakuti Iye amapereka tulo kwa amene amawakonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuli cabe kwa inu Rulawirira mamawa ndi kusagonerapo madzulo, Kudya mkate wosautsa kuupeza; Kuli tero kuti izi apatsa okondedwa ace ngati m'tulo.