Psalms 13:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandiiŵala mpaka muyaya? Kodi mudzandibisira nkhope yanu nthaŵi zonse?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale? Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzandiiwala ciiwalire, Yehova, kufikira liti? Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?