Psalms 130:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, koposa alonda matanda kucha; inde koposa alonda matanda kucha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Moyo wanga umayembekezera Ambuye, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa, inde, kupambana momwe alonda amayembekezera mmawa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Moyo wanga uyang'anira Ambuye, Koposa alonda matanda kuca; Inde koposa alonda matanda kuca.