Psalms 131:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta, mtima wanga ndi wosadzikuza, maso anga ndi osanyada. Sinditengeka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nyimbo yokwerera, ya Davide. Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Salimo la Davide. Inu Yehova, mtima wanga siwodzikuza, maso anga siwonyada; sinditengeteka mtima ndi zinthu zapamwamba ndi zodabwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, mtima wanga sunadzikuza Ndi maso anga sanakwezeka; Ndipo sindinatsata zazikuru, Kapena zodabwiza zondiposa.