Psalms 131:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndautonthoza ndi kuukhalitsa chete mtima wanga, monga mwana amene mai wake amamtonthoza ndi bere. Momwemo mtima wanga uli phe m'kati mwanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma moyo wanga ndawutontholetsa ndi kuwukhalitsa chete ngati mwana amene amayi ake amuletsa kuyamwa, moyo wanga mʼkati mwanga uli ngati mwana amene amuletsa kuyamwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; Ngati mwana womletsa kuyamwa amace, Moyo wanga ndiri nao ngati mwana womletsa kuyamwa.